Mphamvu Now ndi kampeni yomwe ikuchitika pansi pa ndondomeko za mgwirizano wa njira zamakono za mphamvu zotchedwa Green and Inclusive Energy (GIE) motsogoleredwa ndi mabungwe asanu omwe si aboma. Cholinga cha Mphamvu Now ndi kugawa mautenga olondora pankani ya vuto la umphawi wa mphamvu mudziko lathu kupatikiza njila zothandiza kuthetsa vutoli ndi kuphunzitsa aMalawi njira zamakono zosiyana siyana zogwiritsa ntchinto mphamvu zosaononga chilengedwe ndinjila zolumikizana ndi aboma kuti achitepo kanthu pa nkani ya Green and Inclusive Energy.
Mphamvu Now ikufuna kukwaniritsa zolinga zitatu izi;
Kukhazikitsa malo a dijito omwe ndiosavuta kugwiritsa kugwiritsa ntchito pophunzitsa mabungwe, madera komanso anthu za mphamvu
Kulimbikitsa a Malawi m’makomo mwao kuti adziwe komanso kuchitapo kanthu pa nkhani zokhudza mphamvu zosaononga chilengedwe
Kuthandiza kuti zolankhula zokhudza mphamvu zikhale zosavuta kumva kwa a Malawi komanso kuti zikhale mu ziyankhulo za ku Malawi konkuno
Upangiri wodalirika wa dera lanu!
Tili ndi nkhokwe ya zipangizo zomwe zingakuthandizeni kumvetsetsa kwanu kwa malamulo oyendetsera mphamvu kuno Ku Malawi, komanso zipangizo ndi malipoti Omwe mungafune