Kawiri kawiri Mitsinje imatanthauziridwa ngati mbali imodzi ya umoyo yomwe imabweretsa madzi abwino ngakhale ku ma midzi. Kupatula kugwiritsa ntchito madzi pa ntchito monga za nthilira, kuchapira, kusamba, kumwa, kuziziritsa ndi zina mitsinje imapereka mphamvu za kuyenda kwa madzi zomwe zili ndi kuthekera kogwiritsa ntchito kupanga magetsi. Izi zitha kuchitika pa mlingo wa ung’ono pogwiritsa ntchito mphero za mphepo opangidwa ku matabwa ngakhalenso pa mlingo ochuluka pogwiritsa ntchito ma damu akuluakulu.

Zonsezi zikupanga magetsi opangidwa kuchokera ku mphamvu ya madzi kukhala njira imodzi yokhayo yodalirika ku mphamvu za m’bwereza pa dziko lonse la pansi.

Magetsi opangidwa ku mphamvu ya madzi

Kuyankhula mwachindunji, kuyenda kwa madzi kumapukusa makina omwe amapanga mphamvu ya magetsi. Titha kuona kusiyana kwa njira zitatu izi:

Malo opangira magetsi pogwiritsa ntchito damu

 [1]

Damu limapangidwa poyimitsa madzi oyenda ndi cholinga chofuna kupanga malo osungiramo madzi. Madzi amayenda mu paipi yayikulu kuchokera mu damu kupita ku makina opangira mphamvu ya magetsi. Mlingo wa mphamvu ya magetsi utha kupangidwa potengera mlingo kapena kuchuluka kwa madzi komanso kusiyana kwa malupande kuchokera pofikira madzi kufikira kotulukira madzi.

Malo opangira magetsi pogworitsa ntchito damu ndi pampu

 [2]

Kuphatikiza njira yopangira mphamvu  ndi pampu  zimapangitsa njira imeneyi kukhala yamakono chifukwa imatha kufikira kusinthasintha kwa mlingo wa mphamvu yomwe ogula akuifuna. Njirayi ili ndi damu lina lomwe limapezeka kotulutsira madzi. Mu nthawi imene mlingo wa magetsi omwe ukufunika kwa ogula wachepa, mphamvuyi imatha kugwiritsidwa ntchito pokokera madzi kuchoka mu dambo la kumusi kupititsa ku dambo la ku mtunda. Pamene mlingo wa mphamvu ya magetsi omwe ukufunika wachuluka, madzi amatsegulidwa kuchokera ku dambo la kuntunda ndipo magetsi ochuluka atha kupangidwa. 

  

Malo opangira magetsi kuchokera ku mphamvu ya madzi oyenda(Msinje)

 

Madzi amayenda kuchokera ku mtunda kwa mtsinje kupita ku makina opangira mphamvu za magetsi popanda kusungidwa mu. Njira imeneyi ingathe kupewa kuonongeka kwa za chilengedwe komwe kungadze chifukwa kosunga madzi ochuluka malo amodzi. Mlingo wa mphamvu ya magetsi omwe umapangidwa umatengera kayendedwe ka madzi mu nyengo zosiyanasiyana.

[3]

Malo ali onse amene tingapeze madzi oyenda kapena mtsinje, ali ndi kuthekera kokhazikitsapo makina opangira mphamvu za magetsi. Mitsinje ikuluikulu mwa chitsanzo mtsinje wa Congo, Zambezi, Niger, Nile ndi mitsinje ina ing’ono ing’ono yochuluka mu Afrika muno, njira zopangira mphamvu za magetsi kuchokera ku madzi ndizochuluka. Kungoganizira kuti pafupifupi ma peresenti okwanira 90 omwe ali ndi kuthekera kwa mphamvu sanakhazikitsidwe zomwe zikutanthauza kuti pali kuthekera kwakukulu koonjezera makina opangira mphamvu ya magetsi kuchokera ku mphamvu ya madzi. Malo omwe ali ndikuthekera kwambiri akupezeka m’chigawo cha pakati pa maiko a mu Afirika komaso zigawo zina ziliso ndi kuthekera.   

Mphamvu ya magetsi opangidwa kuchokera ku mphamvu ya madzi itha kukhala mma saizi osiyanasiyana:

  • Malo amene kuli makina akulu akulu opangira mphamvu kuchokera ku mphamvu ya madzi ndi omwe amatulutsa mphamvu yochuluka ya magetsi pa dziko lonse ndipo ena mwa iwo ndi makina akulu kwambiri kuposera makina a makono opangira mphamvu ya nyukiliya. Mpamvu yopangidwa kuchokera ku mphamvu yamadzi ndiyo ili yoyenelera kukwanilitsa kufikira mlingo wa ogula maka maka  makampani akuluakulu omwe amagwiritsa ntchito mphamvu yambiri. Pamene makono a ku kulirakulirabe mitengo yopangira mphamvu itha kukhala yotsikirapo mpaka kufika pa mlingo wa ma senti atatu pa chikwi pa ola imodzi mu ndalama ya ku America zomwe zikupangitsa njirayi kukhala yotsikirapo mtengo kusiyana ndi njira zina zopangira mphamvu.
  • Magetsi opangidwa ku makina a ng’ono omwe amapukusa mphamvu ya madzi ocheperako akhoza kukhala a mtengo wa bwino kapena otsikirapo  kwa madera ndi mabanja omwe sanalumikizidwe ndi  nthambo zopereka magetsi pa dziko, (mwachitsanzo, nthambo za ESCOM). Makina ena ndi a ng’ono kwambiri kotero mphamvu ya magetsi yomwe ingapangidwe itha kugwiritsidwa ntchito powunikira pokha ndi ku mvera wayilesi. Kuti mudziwe zambiri onani chithuzi cha makina a ng’ono opukusira mphamvu ya madzi ndi chithuzi cha nyumba kapena malo ogulitsira magetsi.

Ngakhale zili choncho, chimene chikuyenera kuganiziridwa ndichakuti mphamvu yopangidwa kuchokera ku madzi imadalira kwambiri mmene nyengo iliri. Mu nthawi ya chilala pamene mvula siimagwa kwa nthawi yochuluka, mlingo wa madzi mmitsinje umatsika/umachepa komanso mitsinje ina ing’onoing’ono imatha kuumiratu. Mlingo wa madzi oyenda kupita ku makina opangira mphamvu ukachepa, zotsatira zake mphamvu yopangidwa imakhalaso yochepa. Mphamvu ya dzuwa itha kukhala njira yabwino yothandizira mu nyengo imeneyi mlingo wa madzi opangira mphamvu ya magetsi wachepa, (mwachitsanzo nthawi ya chilala).

 

Monga Momwe zanenedwera kale kuti mphamvu yopangidwa kuchokera ku madzi ndi njira yokhayo ya makono yomwe ikugwira ntchito kwambiri ku mphamvu za m’bwereza. M’chaka cha 2015, ma peresenti okwanira 70 a magetsi a m’bwereza anapangidwa kuchokera ku mphamvu ya madzi omwe ali maperesenti okwanira 16.6 pa dziko lonse.  Magetsi opangidwa ku mphamvu ya madzi anayembekezeredwa kukwera ndi ma peresenti okwanira 3.1 pa chaka. Mlingo okwanira 28GW wa kuchuluka kwa mphamvu ya madzi unakhazikitsidwa mu Africa, omwe uli mlingo waukulu pofanizira ndi mphamvu zina za mbwereza monga mphamvu ya dzuwa ndi mphepo ndipo ma pulojekiti ena a mphamvu ya madzi ali nkati momangidwabe.

Malawi imadalira kwambiri mphamvu yopangidwa pogwiritsa ntchito madzi. Pafupifupi maperesenti okwanira 95 pa mlingo omwe unakhazikitsidwa, amapangidwa kuchokera ku makina opukusa mphamvu ya madzi omwe aikidwa m’mbali mwa mtsinje wa Shire. Ngakhale zili choncho, magetsi omwe amapangidwa siokwanira kufikira kwa onse ogula m’dziko muno ngakhale maperesenti okwanira 11 okha a mtundu wa a Malawi ndiomwe alumikizidwa ku nthambo zopereka magetsi. Choncho, kupereka kwa mphamvu kumachepetsedwa malingana ndi kuchulukwa kwa zinthu zimene zikugwiritsa ntchito magetsi zomwe zikutanthauza kuti ma banja ambiri amakhala opanda magetsi kwa maola okwanira 6 tsiku lirilonse (kuthimathima kwa magetsi).

M’nthawi ya chilala nyengo imaipa kapena kusintha kwambiri pamene mitsinje simalandira madzi ochuluka. Kuchepetsedwa kwa kuyenda kwa madzi nthawi zina kumachepetsa mlingo wa mphamvu ya magetsi kufikira pa 200MW. Kusintha kwa nyengo kumaononga kapena kusokoneza nyengo mopyolera muyezo pamene kusinthasintha kwa nyengoku kukuchulukirabe. Kudula kwa mitengo mosasamala komwe a Malawi akuchita kukuonjezera vutoli. Mitengo ndiyofunikira kwambiri pakayendedwe ka madzi: mizu ya mitengo imasunga ndikusamala dothi moyenelera zomwe zimapangitsa madzi a mvula kuyenda ndikulowelera bwino pansi pa nthaka. Popanda mitengo nthaka imauma, kuonongeka ndi kukokoloka zomwe zotsatira zake zimabweretsa kuuma kwa mitsinje ndikuchepetsa kayendedwe ka madzi.

Ngakhale zili chomwecho, boma la Malawi likuonjezera mphamvu zopangidwa kuchokera ku madzi pokhazikitsa makina ena atsopano. Kukhazikitsa kwa makina ena a mphamvu atsopanowa monga Mpatamanga mu mtsinje wa Shire ndi imodzi mwa ma pulani atsopano ofuna kuchepetsa mavuto a mphamvu omwe alipo.

Mukhoza kudziwa zambiri pa nkhani zina ndi zina zofunukira zokhudza mphamvu za m’bwezera popita pa webusaiti ya: www.conrema.org