Mbaula

Home > Mbaula

Boma la Malawi lazindikira njira yothandiza kuchepetsa kuonongeka kwa chilengedwe po khazikitsa ma pulani a nthawi yayitali ogawa mbaula za makono zosaononga chilengedwe zokwanira ma miliyoni awiri pofika m’chaka cha 2020. Pali mbaula za makono zosiyanasiyana kuyambira zotsikirapo mtengo zomwe zili zosavuta magwiritsidwe ntchito ake ndi zina zomwe zili zovutirapo magwiritsidwe ntchito ake.

Mbaula zina zosaononga chilengedwe zimagwiritsabe ntchito nkhuni ndi Makala koma ndi zabwino ndi zosaononga chilengedwe kusiyana ndi mbaula za makolo zomwe ndi mafuwa atatu komanso Mbaula zomwe zimononga chilengedwe. Izi zikutanthauza kuti mbaula zosaononga chilengedwe zimagwiritsa ntchito mbali yayikulu ya mphamvu yomwe ikufunika ndikuononga mphamvu yochepa. Kagwiritsidwe ntchito kabwino ndi kosaononga kali ndi zotsatira zambiri:

  • Kuteteza Nkhalango: Kugwiritsa ntchito nkhuni zochepa, izi zikutanthauza kuti mitengo yochepa ndiyomwe imadulidwa. Izi zichepesa kuonongeka kwa mitengo ya nkhalango zathu ndipo pakapita nthawi, chonde cha m’nthaka yathu chima onjezereka.
  • Kusunga ndalama ndi nthawi. Kugwiritsa ntchito ndalama yochepa pogula Makala ndi nkhuni. Kugwiritsa ntchito nthawi yochepa yotolera kapena kuyang’ana nkhuni. Ndi nthawi yochepa imene imagwiritsidwa ntchito potolera nkhuni, oyang’ana kapena kutolera nkhuni maka maka amayi ndi ana atha kugwiritsa ntchito nthawi imeneyi pochita zinthu zina zothandiza zomwe zitha kutukula ma banja awo.
  • Ku teteza moyo. Zimatulutsa utsi ndi mpweya oipa ochepa zomwe sizingaike moyo pa chi opsyezo. Pamakhala chiopsyezo chochepa cha ngozi ya moto.

Mbaula zina zosaononga chilengedwe zimagwiritsa ntchito mafuta kapena nkhuni za bwino monga zinyenyeswa za nkhuni zomwe zimaumbidwa ngati mbamu kapena mafuta oyengedwa ku zinthu zoola zomwe zilibe mavuto akulu/zomwe zili ndi ubwino ochuluka.

  • Mbaula zo umbidwa ndi dongo, mwa chitsanzo, Chitetezo mbaula, mbaula ya ‘’Wina Alira’’, Mbaula ya Aleva.
  • Mbaula ya uvuni yomangidwa ndi dongo yomwe itha kukhala ndi khomo limodzi kapena makomo angapo imagwiritsa ntchito nkhuni zochokera ku zomera. Mwa chitsanzo, mbaula ya uvuni yakhomo limodzi, ‘’Changu Changu Moto’’ Mbaula ya Roketi, mbaula ya Roketi ya Total Land Care (TLC).
  • Mbaula za malate zomwe zimagwiritsira ntchto nkhuni zosiyanasiyana zochokera ku zomera kapena zogwiritsa ntchito zinyenyeswa za nkhuni ndi zinyalala zoumbidwa ngati mbamu. Mwa chitsanzo mbaula yosavuta manyamulidwe ya roketi, mbaula ya Mwanaleza
  • Mbaula ya makono yogwiritsa ntchito nkhuni zochokera ku zomera. Mwa chitsanzo, Ezy mbaula: mbaula yomwe imagwiritsa ntchito nkhuni zochokera ku zomera komaso mphamvu ya dzuwa.
  • Mbaula zimene zimagwiritsa ntchito kachasu ngati mafuta
  • Mbaula zogwiritsa ntchito mpweya opangidwa kuchokera ku mafuta omwe amayengedwa ku zinthu zoola
  • Mbaula zogwiritsa ntchito mpweya opangidwa ku zinthu za moyo zoola.

Zinthuzi za mbaula zosaononga chilengedwe zomwe zikupezeka m’ma dera a ku Malawi

Chitetezo Mbaula

Chitetezo mbaula ndi imodzi mwa mbaula zosaononga chilengedwe imene ili yodziwika m’Malawi. Imapangidwa ndi dothi la dongo lomwe mtengo wake ndi osaboola mthumba ndipo ndiyosavuta kupanga kwake maka ku ma dera osiyanasiyana m’Malawi muno.

  • Zipangizo: Dongo. Dongo limapezeka m’ma dera ambiri osiyana siyana m’Malawi, koma kupeza dongo loyenelera ndi kovutirapo.
  • Zipangizo ndi maphunziro: zimafuna zikombole zoyenera ndi maphunziro a pa dera kuti mbaula ipangidwe mwa makono; chikombole chofuna mphamvu ndichomwe chili choyenelera kuti mbaula ipangidwe mwa makono; nkhuni ndi nyumba yootchera mbaula.
  • zimatenga pafupifupi ma sabata atatu kapena anayi kuti ipagidwe
  • Itha kupangidwa motsika mtengo ndi mosavuta maka kwa magulu ochita za malonda a ng’ono ang’ono.
  • Ndizosalemera kapena zosavuta manyamulidwe ndi masungidwe
  • Ndi zosaboola m’thumba komaso zosavuta kugwiritsa ntchito
  • Nkhuni: Mitundu yosiyanasiyana ya zomera kapena nkhuni, mwa chitsanzo, tizidutswa ta nkhuni ndi ndodo, zinyalala za zokolola monga zisononkho, mapesi, ndodo za nandolo ndi zina
  • Zimachepetsa magwiritsidwe ntchito a nkhuni mpaka kufikira ma peresenti asanu.
  • Imadyetsa anthu pafupifupi khumi ndi awiri, koma siyoyenera kuphikirapo kapena kugwiritsa ntchito ma poto akulu akulu.
  • Imatha kukhala ndi n’galu pa mwamba ukayamba kugwiritsa ntchito zomwe zimakhudza maonekedwe ake koma izi zisikhudza magwiridwe a ntchito yake.
  • Zimafunika munthu amene ali ndi luso lokonza mbaula kuti akonze pamene yaonongeka.
  • Mtengo ogulitsira: Unayambira 800 kwacha mpaka 2,000 kwacha
  • Kugwiritsa ntchito moto kapena mphamvu mosamala ndi mosaononga (ndi mlingo uti wa mphamvu omwe ungapangidwe kuti ugwiritsidwe ntchito potenthetsera poto). Mongoganizira chabe, (maperesenti okwanira makumi atatu ndi theka kusiyanitsa ndi maperesenti okwanira khumi limodzi a mafuwa atatu) chifukwa cha kutukuka kwa kayakidwe komaso kusintha kwa katenthedwe ka mbaula.
  • Kutulutsa: Zimatulutsa mpweya oipa ochepa pafupifupi maperesenti osafika makumi anayi ndi mphambu zisanu komaso  utsi ochepa osafika ma peresenti makumi anayi ndi mphambu zisanu ndi imodzi kusiyanitsa ndi kugwiritsa ntchito mafuwa atatu.  
  • Kusunga mitengo: Kuchepetsa kagwiritsidwe ntchito ka nkhuni pafupifupi maperesenti makumi asanu izi zikutanthauza kuti Chitetezo Mbaula imodzi imapulumutsa mitengo isanu ndi umodzi pa chaka.

Aleva Mbaula

Mbale zokwanira khumi ndi mphambu zinayi zopangidwa ku chokera mu dongo, mchenga wa ku mtsinje ndi simenti zimagwiritsidwa ntchito pamodzi popangira mbaula imeneyi.

  • Zipangizo: dongo, mchenga wa ku mtsinje ndi simenti
  • Mbaula ikapangidwa imaumitsidwa ndi mphepo ndipo simafunika kuiotcha
  • Mbale nkhumi ndi zinayi (14) (zisanu ndi zitatu (8) zimaikidwa pansi pamene zisanu ndi imodzi (6) zimaikidwa pa mwamba) zimaikidwa pamodzi kupanga mbaula. Malatawa amaonjezera kulimba ndi kukhazikika kwa mbaula.
  • Zipangizo ndi maphunziro a padera: Zimafuna zikombole zochuluka zosiyanasiyana, ndi zipangizo zodilizira komaso zoyezera popanga mbaula.
  • Munthu m’modzi opanga mbaula akhoza kupanga mbaula ziwiri (2) pa tsiku.
  • Ndiyosavuta kunyamula pa nthawi imene zipangizo za mbaula zisanalumikizidwe, koma ndiyolemera komaso ndiyovuta kunyamula pa nthawi imene mbaulayi yalumikizidwa kapena kukonzedwa.
  • Ndiyosaboola mthumba komaso yosavuta kugwiritsiraa ntchito
  • Ndiyosayenera kugwiritsa ntchito mapoto akulu akulu.

Mbaula ya Changu Changu Moto

Imamangidwa pa malo a modzi pogwiritsa ntchito zipangizo zosavuta kupeza ndipo imakhala ndi magawo ophikira angapo.

  • Ndizosaboola mthumba komaso zosavuta kupanga
  • Zipangizo zake ndizosavuta kupeza monga dongo, mchenga ndi ndowe za ng’ombe
  • Imayamba kugwiritsidwa ntchito pakangotha masiku awiri kapena atatu itapangidwa.
  • Ndiyovuta manyamulidwe
  • Itha kuphikilidwa mapoto awiri kapena atatu pa nthawi imodzi, magawo awiri a mbaula amapereka mwayi ochuluka ogwiritsa ntchito.
  • Ndiyosavuta kukonza ikaonongeka
  • Imaonongeka mosavuta komaso malo oika poto amaonongeka mosavuta.
  • Ndiyosayenera kugwiritsa ntchito ma poto akuluakulu

Mbaula ya Total Land Care (TLC)

Mbaula ya gawo limodzi yopangidwa ndi matope, yokonzedwa mwa makono ndi zoimikira za matabwa, zitsulo ndi zogwirizira ma poto.  

  • Ndiyosavuta mapangidwe ake komaso ndiyosaboola mthumba
  • Imatha kugwiritsidwa ntchito pakatha masiku awiri kapena atatu ikatha kupangidwa
  • Ndiyovuta manyamulidwe
  • Ndiyo pangidwa mwa makono pogwiritsa ntchito zitsulo ndi matabwa komaso zoimikira ma poto.