Kuyenda ndi mphamvu. Chinthu chimodzi chomwe chimayenda mwa chilengedwe pa dziko lonse ndi mpweya: mphepo. Mphamvu yochokera mu mpweya itha kulumikizidwa ku makina omwe amapukusidwa ndi mphepo. Mphamvu yochokera mu kuyenda kwa mpweya itha kugwiritsidwa ntchito popereka mphamvu ku makina ena monga ma pampu kapena kupukusira makina opangira mphamvu ya magetsi.   

Magetsi a mphepo

Mphepo imapukusa makina. Kenako amayendetsa genelata yomwe imapanga magetsi ndipo magetsiwa amatumizidwa ku nthambo zopereka magetsi ngakhale m’nyumba. Onani chithuzi chili m’musimu:

Tikhoza kusiyanitsa pakati pa makina opukusa mphepo ya pa mtunda ndi makina opukusa mphepo ya pa nyanja potengera malo  

Mphepo ya pa mtunda

Kupanga magetsi kuchokera ku mphepo ya pa mtunda ndikotsikirapo mtengo zomwe zikupangitsa njirayi kukhala yopikisana ndi njira zina zopangira mphamvu ya magetsi. Njirayi imagwiritsidwa ntchito kupanga mphamvu yochuluka ngakhaleso yochepa.

  • Minda yaikuluikulu ya makina opukusa mphamvu ya mphepo ndi makina ambiri  opukusidwa ndi mphepo omwe amapereka mphamvu ya magetsi ku nthambo zolumikizana za magetsi pa dziko.onani chithuzi chili m’musimu (onani chitunzi mmusimu).
  • Mongoonjezera, makina a ng’ono opukusidwa ndi mphamvu ya mphepo amapereka magetsi ku madera kapena nyumba zomwe sizinalumikizidwe ku nthambo zopereka mphamvu ya magetsi pa dziko: onani zithuzi za makina a ng’ono, nyumba yopereka magetsi ndi magetsi operekedwa pa nyumba

Mphepo ya pa Nyanja

[2]

Mphepo ya pa Nyanja ndi ya mphamvu komaso yokhazikika kusiyana ndi mphepo ya pa mtunda zomwe zikutanthauza kuti magetsi ambiri atha kupangidwa. Koma, mtengo okhazikitsira ndi kukonzera makina opukusira mphamvu ya mphepo ya pa Nyanja ndiokwera kwambiri.

Tikayang’ana kuthekera kwa mphamvu ya magetsi opangidwa kuchokera ku mphamvu ya mphepo mu Afirika muno, ndikochuluka kuposera mulingo wa ogula. Izi zikutanthauza kuti mulingo wa magetsi omwe ukufunikira ukanatha kufikiridwa pogwiritsa ntchito mphamvu ya mphepo yokha. Ma peresenti okwanira 15 a mphamvu ya mphepo mu Afirika muno ndi a makono zomwe zikutanthauza kuti titha kupanga magetsi ochuluka motsika mtengo ndi mphamvu zochepa.

Mphepo simwazikana mofanana m’madera ngati momwe kuchitira kunyezimira kwa dzuwa, koma izi zimatha kuchitika m’madera okhawo amene ali ndi kuthekera kogwiritsa ntchito mphamvu ya mphepo. Dziko la Malawi ndi limodzi mwa maiko a ku m’mawa kwa Afirika omwe ali ndi magwero a bwino a mphamvu ya mphepo. Choncho, dziko liri lonse liri ndi mphamvu ya mphepo yosinasiyana potengera malo osiyanasiyana monga m’mbali mwa Nyanja ndi kuyalana kwa mapiri. Makina opukusidwa ndi mphamvu ya mphepo asanakhazikitsidwe, pamakhala kuyeza kapena kuunika kaombedwe ka mphepo kwa pafupifupi chaka ndi cholinga chofuna kupeza malo oyenelera odutsa mphepo.

Mphepo yodutsa pa mtunda imasinthasintha kwambiri kwa nthawi yochepa: tsiku lina mphepo itha kukhala yochuluka ndipo mphamvu yambiri itha kupangidwa pamene tsiku lina mphepo itha kukhala yocheperatu yoti singapukuse makina opangira mphamvu ya magetsi. Choncho, mphamvu yopangidwa kuchokera ku mphepo imaphatikizidwa ndi mphamvu zina monga mphamvu ya dzuwa kapena kukhazikitsidwa pamodzi ndi uyang’aniri wa mphamvu zina monga kuchita mgwirizano wa malonda ndi cholinga chofuna kupeza mphamvu zodalirika. 

Kasakaniza wa mphamvu ya mphepo ndi mphamvu ya dzuwa

M’chaka cha 2017, mphamvu ya magetsi yopangidwa kuchokera ku mphepo inakwera ndikufikira ma peresenti okwanira 4.4 pa dziko lonse. Mu Afirika, mulingo wa mphamvu yopangidwa kuchokera ku mphepo omwe unakhazikitsidwa unali okwanira pafupifupi 4.5 miliyoni watsi (4.5MW) koma pafupifupi theka la mphamvuyi inapangidwa mu dziko la South Africa. Kupatula dziko limeneli, maiko ena monga Egypt, Morocco, Ethiopia ndi Tunisia anatengaposo mbali yofunikira kwambiri.

Dziko la Malawi siligwiritsa ntchito njira ya mphamvu ya magetsi a mphepo. Kwakhala kukuchitika kafukufuku wa mphamvu ya mphepo m’madera osiyanasiyana a m’dzikoli zaka zapitazo ndi cholinga chofuna kupeza malo omwe ali ndi kuthekera. Malingana ndi nthambi yoona za mphamvu, ma pulani awo ndiokhazikitsa minda ya mphamvu ya mphepo mtsogolo muno, njira imene ikuonetsa kukhala njira ya mphamvu yotsikirapo mtengo ndiyosaononga chilengedwe yomwe itha kukhazikitsidwa kwa nthawi yochepa. Choncho, njirayi imaonedwa ngati yaying’ono yongoonjezera ku mphamvu yopangidwa ku madzi kotero sipamakhala chidwi kwenikweni chogwiritsira ntchito njirayi.

Khalani odziwa zambiri pa nkhani zofunikira zosiyanasiyana zokhudza mphamvu za m’bwezera poona pa webusayiti iyi www.conrema.org!