Katundu wopezeka ku Malawi

Nyali zing’ono zing’ono ngati poyambira

Nyale yowerengera ya A1:

  • Mbale yotenga mphamvu yadzuwa yolumikizidwa
  • Maola anayi akuwunikira
  • Zosalemera, zonyamulika, zolimba komanso zokhala ndi zogwilira zosunthika
  • Chaka chimodzi cha mwayi wogwiritsa ntchito komanso zaka zitatu zogwiritsa ntchito batire
  • Mtengo pafupifupi MK4,000.00

Nyali yowerengera ya S2/S3:

  • Mbale yokola mphamvu yadzuwa yolumikizidwa pamodzi ndi nyali
  • Maola anayi a kuwala kwambiri
  • Yopepuka, yonyamulika, yolimba komanso yokhala ndi zogwirira zosunthika
  • Zaka ziwiri za mwayi wogwiritsa ntchito komanso zaka zisanu zogwiritsa ntchito batire
  • Mtengo pafupifupi MK7,500.00

Nyali yowerengera ya SM100:

  • Mbale yokola mphamvu yadzuwa yolumikizidwa limodzi ndi nyali
  • Maola oposa asanu owunikira
  • Nyali yoyika patebulo, kupachikidwa komanso kuunikira
  • Chaka chimodzi chogwiritsa ntchito komanso zaka zisanu zogwiritsa ntchito batile

Makina a Sun King Pico:

  • Mbale yokola mphamvu yadzuwa yolumikizidwa limodzi ndi nyali
  • Maola owunikira mpaka makumi asanu ndi awiri ndi mphambu ziwiri
  • Yokhala ndi zogwirira zosunthika
  • Zaka ziwiri zamwayi wogwiritsa ntchito
  • Mtengo pafupifupi MK6,500.00

Nyali za King Eco:

  • Mbale yadzuwa yotulutsa mphamvu zokwana wati imodzi, yotchingiridwa ndi chitsulo cha aluminiyamu, yotetezedwa ndi galasi komanso yokhala ndi waya otumizira zinthu
  • Mpaka maola makumi atatu a kuunikira ndiponso yokhala ndi milngo itatu ya kawalidwe
  • Itha ku kupachikidwa pamwamba kapena kuyikidwa pa desiki
  • Zaka ziwiri za mwayi ogwiritsa ntchito komaso mpakana zaka zisanu zogwiritsa ntchito batire
  • Mtengo Pafupifupi MK8,000.00

Nyali zowerengera za d.light S20:

  • Mbale za mphamvu yadzuwa zolumikizidwa kumodzi ndi nyali
  • Mpaka maola asanu ndi atatu owunikira komanso mlingo wakakwezedwe ka kuwala kuwiri
  • Mlingo wa madigiri 360 ozungulira potsalilira kuwala
  • Yopepuka ndi yopangidwa monyamulika komaso yazigwilirao zusunthika
  • Zaka ziwiri za mwayi ogwirtsa ntchito kuphatikizapo batire lokhala dzaka zisanu
  • Mtengo pafupifupi MK9,000.00

Nyali zamphamvu yadzuwa za TD100:

  • Mbale zokola dzuwa zapaderadera zopanga mphamvu yokwana ma wati 1.2
  • Mpaka maola asanu ndi atatu owunikira komanso kuwala kwa milingo iwiri
  • Nyali zopangigwa kuti zithe kunyamulika komanso kupachikidwa pamwamba
  • Zaka ziwiri za mwayi zogwiritsa ntchito

Makina a Team Planet Linesman Bright:

  • Imankhala ndi nyali, malo olumikizira nthambo yomwe imatumizira uthenga, tizigwiriro tiwiri topachikira ndipo simakhala ndi mbale yokola mphamvu yadzuwa
  • Mbale yokola dzuwa yokhala payokha komanso chipangizo chosungila moto wamphamvu zalimgo wosiyanasiyana
  • Maola oyambila pa awiri mpaka makumi asanu ndi awiri potengera ndi mlingo wakayakidwe, malo okhala ndi pounikira okwana asanu
  • Nyali ya ma lumeni okwana 180

Nyali za Team Planet Striker:

  • Imakhala ndi nyali, nthambo zotumizira uthenga, chimangiririra chimodzi ndipo simabwera ndi mbale yakeyake yokola mphamvu dzuwa.
  • Mbale yokola dzuwa yokhala payokha ndi malo osungila moto wamagetsi
  • Kuyaka kuyambila maola asanu ndi imodzi kufika maola khumi ndi anayi ndi kuwala kwamlingo uwiri
  • Yokhala ndi malumeni 150

Nyali zatchedwa Planet Linesman Magnetic:

  • Imakhala ndi kuwala, malo olumikizira nthambo zotumizila katundu, zingwe ziwiri zopachikirira zapadera ndipo imakhala yopanda mbale yokola mphamvu ya dzuwa
  • Mbale zokola dzuwa yokhala payokha ndi chipangizo chosungira moto
  • Malo asanu amlingo owunikira
  • Nyali ya malumeni 180
  • Imamatiliridwa ndi zitsulo
Nyali za ukadaulo wapaderadera

Sun King Pro ‘All Night’:

  • Nyali yowunikira komanso kutchajira mafoni
  • Mbale yapadera yokola mphamvu yadzuwa yokwana ma wati 2.7
  • Mpaka maola 45 owunikira ndi mlingo utatu wa kuwala (kokhala ndi ma lumeni 17, 50 komanso 100)
  • Yokhala ndi zogwirizira zomwe zimatha kuchotsedwa
  • Malo otchajira mafoni
  • Zaka ziwiri za mwayi ogwitsa ntchito ndi moyo wa batire wa zaka zisanu
  • Mtengo pafupifupi MK29,000.00

Nyali ya d.Light-S300:

  • Nyali yowunikira komanso malo otchajira mafoni
  • Mbale yakola mphamvu yadzuwa yokwana ma wati atatu komanso waya wamtali a mamita anayi
  • Mpaka maola 100 akuwala ndi kuwala koyikidwa pa milingo inayi
  • Kuwala kwa nyali kosinthidwa pa ngodya zochulukirapo
  • Malo olumikizira nthambi zosamutsira uthenga
  • Zaka ziwiri za mwayi wogwiritsa ntchito komaso dzaka zisani za umoyo wa batire
  • Mtengo pafupifupi MK25,500

Sun King Pro 400:

  • Mbale yokola moto wamagetsi wamphamvu zokwana ma wati 5.5 komanso ndi waya wa mamita asanu
  • Maola asanu owunikira pa malumen 400 komanso maola 100 pa malumen 25
  • Imagwira ntchito bwino kwambiri
  • Imakhala ndi zinthu zotchajira mafoni
  • Mwayi wazaka ziwiri zogwiritsa ntchito

Sun King Boom:

  • Mbale zokola mphamvu yadzuwa yokwana ma wati 2.7 komanso waya okwana ma mita asanu
  • Maola 6 owunikira pa nyali yama lumeni 160 komanso maola 36 owunikira pa malumeni 25
  • Yokhala ndi wayilesi ya digito komanso sipika ya wayilesi
  • Imakhamaso ndi katundu wotchajira mafoni
  • Zaka ziwiri za mwayi ogwiritsa ntchito

ovPilot X/op Solar:

  • Mpaka maola 8.5 owunikila ku nyali pama lumeni 74 komanso maola 45 ku nyali pama lumeni 12
  • Kuthekera kwamkatikati kotchanja mafoni
  • Kupereka kuwala kosathobwa mmaso
  • Zaka ziwiri za mwayi wogwiritsa ntchito
Zipangizo zobwera limodzi ndi nyali

Beacon MB2-200:

  • Zipangizo monga: nyale imodzi ndi tchaja cha phone komanso ka tochi konyamulika
  • Mbale yokola mphamvu yadzuwa yapaderadera yokwana ma wati 2.8
  • Milingo itatu ya kawalidwe: maola asanu owunika pa mlingo owala kwambiri, maola khumi a kuwala kwa sayizi yabwino, maola 100 pamlingo wa maola 100
  • Malo olumikizira nthambo yotumizira uthenga
  • Mwayi wachaka chmodzi chogwiritsa ntchito
  • Mtengo pafupifupi MW30,500

Beacon ovSolar Marathoner MB160:

  • Katundu ngati nyali imodzi yokhala ndi malo otchanjira mafoni komanso tochi
  • Mbale yokola mphamvu yadzuwa yapaderadera yokwana ma wati 2.5
  • Milingo itatu yakawalidwe: kuwala kwambiri pama lumeni 160, maola 150 owunikira pamlingo waung’ono
  • Malo olumikizira nthambo yotumizira zinthu
  • Zaka ziwiri za mwayi wogwiritsa ntchito

Marathoner MB 2-290:

  • Katundu ngati nyali ziwiri, tochi yonyamulika, malo olumikiza nthambo yotumizila uthenga
  • Mbale yokola mphamvu yadzuwa yokwana ma wati anayi
  • Mlingo wakawunikidwe ka mlingo itatu, maola 5 akuwala kwambili, maola 12 akuwala kwapakatikati ndi maola 150 akuwala kwa mlingo kocheperako
  • Zaka ziwiri za mwayi wakugwiritsa ntchito
  • Mtengo pafupifupi MK102,000.00

Nyali za D20:

  • Makina amakhala ndi nyali ziwiri zomwe zitha kupachikidwa pakhoma, nyali imodzi yonyamulika, malo olumikizira nthambo yotumizila thenga ndi kutchanjira zinthu
  • Mbale yokola mphamvu yadzuwa yapaderadera komanso nthambo yotalika ma mita asanu ndi imodzi
  • Mpaka maola nkhumi ndi asanu owunikira
  • Mtengo pafupifupi MK80,000.00

Ubwino wa nyali zogwiritsa ntchito mphamvu yadzuwa

Nyali zogwiritsa ntchito mphamvu yadzuwa zimakhala zowala kwambiri kutithandizira kuti tigwire ntchito usiku mosavuta. Itha kugwiritsa ntchito kuwerengera kapenanso kuchezera.

Ilibe zovuta chifukwa cha kuyaka chifukwa sikhala ndi kaboni woyipa wowononga umoyo wa anthu ndi zachilengedwe

Pali mwayi omwe umaperekedwa kuti athu azitha kupereka ndalama uku akugwiritsa ntchito (kupereka kumakhala kwa pang’onopang’ono pofanana ndi mmene ma kandulo angagulidwire pa nthawi yayitali mpakana mtengo ogulira utafikiridwa). Pamene nyali yamphamvu yadzuwa imeneyi yagulidwa, imagwiritsidwa ntchito popanga ndalama ina yoonjezera. Sitiyeneranso kugula makandulo kapena nyali zoyenera mafuta. Nyalizi sizikhala ndi mtengo uliwonse chifukwa zimagwiritsa ntchito mphamvu dzuwa.