Report by Caroline Kachipapa,edited by Kenneth Mtago
Ngati njira imodzi yofalitsira uthenga wokhudza kasamalidwe ka chilengedwe komanso kumemeza anthu kugwiritsa ntchito mphamvu ya m’bwezera, bungwe la Renew’N’Able Malawi (RENAMA) likuchititsa masewero ampira wa miyendo komanso wamanja pakati pa sukulu za sekondale zokwana zisanu ndi zitatu m’madera a Lunzu komanso Chileka mu mzinda wa Blantyre.
Masewerawa, akutchedwa GIE Sports Bonanza akuchitika ndi chithandizo chochokera ku bungwe HIVOS pansi pa ntchito ya Green and Inclusive Energy (GIE) yomwe ikutchedwa kuti Mphanvu-Now. M’mawu ake Ogwira ntchito yolimbikitsa za GIE a Kenneth Mtago anati, bungwe la RENAMA likuchititsa masewerawa ngati njira imodzi yofuna kufalitsira uthenga wa mphamvu ya m’bwezera, yomwe ndi mphamvu yokhalitsa komanso ya ukhondo yomwe sibweretsa matenda pa umoyo wa munthu.
“Imeneyi ndi ntchito imodzi yomwe bungwe la RENAMA likugwira ndi cholinga choti anthu alandire uthenga wokhudzana ndi kusintha kwa nyengo komanso ndi mmene akhudzidwira ndi umphawi wa mphamvu komanso mu ntchito za chitukuko za Dziko”, watero Mtago.
“Bonanza iyi ndi njira imodzi yowatengera anthu chifupi ndi uthenga omwe tili nawo ndikuti tithe kuwagawira uthenga umenewu kudzera mu chinthu chomwe amachikonda chomwe ndi masewera ampira wamiyendo komanso wamanja”.
A Mtago anaonjezeranso kuti, bungwe la RENAMA lasankha kufalitsa uthenga m’madera a Lunzu ndi Chileka chifukwa awa ndi ena mwa Madera omwe akukhudzidwa kwambiri ndi vuto lodula mitengo ndinso kuotcha makala mwachisawawa. A Mtago anati, iwo ndi okhutira ndi momwe anthu akubwerera kudzaonera masewerawa, izi malingana ndi a Mtago, zapereka chiyembekezo chachikulu ku bungwe lawo kuti uthenga ukufikira bwino lomwe kwa anthu.
Kupatula mwai owonera mpira wamiyendo komanso wamanja, anthu ali ndi mwai opata mphatso zosiyana siyana monga zipewa, ma Tshirt ndi zina zomwe zalembedwa uthenga owakumbutsa komanso kuwalimbikitsa kugwiritsa ntchito mphamvu za m’bwezera.
Masewera a mpira omwe anachitika Loweruka pa 26 October 2019 pa Chikuli ground , komanso la Mulungu pa 27 October 2019 pa Lunzu primary School ground komanso Lunzu secondary school ground anaseweredwa ndi ma timu okwanira asanu ndi atatu.
Ku Chileka, masewera a mpira wamiyendo, timu ya Chigumukire CDSS yafika mu ndime yama timu anayi (semi finals) itagonjetsa timu ya Chikuli CDSS ndi zigoli zinayi kwa chimodzi (4-1) ndipo timu ya St. George yafika mu ndime yama timu anayi itagonjetsa Chilangoma CDSS ndi zigoli ziwiri kwa duu (2-0).
Masewera a mpira wa manja timu ya Chigumukire CDSS yafika mu ndime yama timu anayi (semi finals) itagonjetsa timu ya Chikuli CDSS ndi zigoli khumi kwa duu ndipo timu ya St.George Academy yafika mu ndime yama timu anayi (semi finals) itagonjetsa timu ya Chilangoma CDSS ndi zigoli 15 kwa 13.
Ku Lunzu, masewera mpira wa miyendo, Timu ya Lunzu secondary school yafika mu ndime yama semi finals itagonjetsa timu ya Trinity Acadamey ndi zigoli zisanu ndi chimodzi kwa ziwiri ndipo Timu ya Ngumbe Secondary School yafika mu ndime ya semi finals itagonjetsa Timu ya Amazing Grace ndi zigoli zinayi kwa ziwiri.
Masewera a mpira wa manja, timu ya Amazing Grace Academy yafika mu ndime yama Timu anayi (semi finals) itagonjetsa timu ya Ngumbe secondary school ndi zigoli 25 kwa 14, ndipo timu ya Trinity Academy yafika mu ndime yama Timu anayi itagonjetsa timu ya Lunzu Secondary School ndi zigoli 16 kwa 12.
Masewera a ndime yama timu anayi (semi finals) akuyembekezereka kuseweredwa loweruka pa 02 November 2019 pa bwalo lamasewero la Lunzu Primary School ndi Chikuli ku Chileka.
Masewera a mpira wa miyendo, timu ya Chigumukire CDSS ikuyembekezera kudzasewera ndi St. George Academy, ndipo Lunzu Secondary School ikuyembekezera kudzasewera ndi Ngumbe Secondary School.
Masewera a mpira wa manja, timu wa Chigumukire CDSS ikuyembekezera kudzasewera ndi St. George Academy, ndipo timu ya Amazing Grace Academy ikuyembekezera kudzasewera ndi Trinity Academy.