Zophikira zimene zimachokera ku zomera ndi zithu zimene zimachokera ku zomwe zidakhalako ndi moyo komanso zamoyo, izitu zitha kukhala zomera komanso nyama. Titha kugwiritsa ntchito mphamvu zimene zili mu nkhuni, zotsalira zochokera ku nkhuni, zochokera ku mbewu, manyowa komanso nzimbe pakugwiritsa ntchito mafuta omwe amapezeka mu zomerazi. Zinthu zochera kuzomera zimatulutsa mphamvu nthawi yomweyo kuchoka ku zomera ndipo zina zimathaso kukhala zinthu zimene zimatsalira kuchoka ku zomera zakumunda, pakhomo komanso mma kampani. Kutenga mphamvuzi pamafunika kuotcha zomerazi kapena kuzisintha kupita munjira zina ngati zolimba, zamadzimadzi komanso zonga ngati mpweya mwachitsanzo mpweya omwe umapangidwa zinthu zikamawola, mafuta a dizilo omwe ndi mtundu wamowa wa kachasu omwe umatha kugwiritsidwa ntchito kuyendesera galimoto. Mphamvuzi zitha kugwiritsidwa ntchito pakuphikira, kutenthetsa zinthu, kuyendetsera magalimoto komanso kupangira magetsi.

Mafuta omwe amapangidwa kuchoka ku zomera amakhala ndi mpweya wa kaboni opanda mbali ndipo mpweya oyipa opezeka mulengalenga umene umatumizidwa kuchoka mu kuyaka kwazinthu ndiofanana ndi mlingo umene umatengedwa ndi zomera. Komabe m’Malawi mmuno izi sizili choncho.

Mphamvu zophikira/kuunikira kuchokera kuzomera

Mmene zinthu ziliri ku Malawi

Kuphikira ndi njira imene mphamvu imagwiritsidwa ntchito mowirikiza m’nyumba zambiri kuno ku Malawi. Ndipo kufunika uku kumagwiritsidwa ntchito ndi mphamvu yochoka ku zomera ngati Makala komanso nkhuni. Nkhuni ndi njira yaikulu imene mphamvu zimagwiritsidwa ntchito ku Malawi, kusiyana ndi magetsi adziko amene amagwiritsidwa ntchito pamlingo wochepa.

Ku madera akumudzi kuphikira kapena kugwirirtsa ntchito nkhuni ndi njira yomwe imagwiritsidwa kawirikawiri pamene mmadera akutawuni anthu amakonda kugwiritsa ntchito Makala.  Njira imene imagwiritsidwa ntchito kwambiri ndi kuphika kugwiritsa ntchito mafuwa atatu imene ili yosadalirika, zimatenga nkhuni zambiri koma moto umene umagiritsidwa ntchito umakhala ochepa, motsogozedwa ndi mbaula zogwiritsa ntchito Makala. Kupatula kugwiritsidwa ntchito m’makomo, amalonda komaso ma kampani amene ali minda ya tea komanso malo opanga njerwa zimadaliranso nkhuni.

Kugwiritsa ntchito nkhuni ndi makala ndi njira zimene zili zosakhazikika komanso zoononga chilengedwe pakakhala kuti mitengo sikudzalidwaso. Mphamvu zochoka mu zomera ndi zinthu zimene zikuthandizira kuonongeka kwa mitengo m’dziko muno, zimenezi zimabweretsa zotsatira zoyipa mu nthaka ngakhaleso kuposera apo monga kusintha kwanyengo, kuyenda mitunda italiitali kusaka nkhuni komanso kuchepa kwa mlingo wamagetsi chifukwa cha kuchepa kwa kuthekera kwamitsinje yathu. Makala amaonjezeranso kuonongeka kwambiri kwa nkhalango chifukwa mtengo umodzi umapanga thumba limodzi la Makala pamene ngati wapangidwa nkhuni utha kutulutsa matumba khumi.

Kuchotsera apo, kugwiritsa ntchito makala ndi nkhuni zimayika moyo wa anthu pachiwopsezo. Izi, zili chomwechi chifukwa cha mpweya oyipa omwe umatulutsidwa komanso mchitidwe wankhaza monga wogwililira umene umachitika pamene azimayi ndi asikana  akayenda mitunda yaitali kusaka nkhuni.

Zophikira zochokera ku zomera ndi njira yaikulu yomwe mphamvu zimachokera muno m’Malawi. Apatu ndi pamene dziko la Malawi lingayambe kugwiritsa ntchito mphamvu zina monga za m’bwezera.

Njira Zodutsamo

Titha kugwiritsa ntchito njira ziwiri kuti tichepetse zotsatira zomwe zimabwera mu kugwiritsa ntchito zophikira zochoka ku zomera zosakakhazikika komanso zoononga chilengedwe.

1.

Kugwiritsa ntchito nkhuni kumatha kupangidwa kukhala kwabwino komanso kopindula ngati tingagwiritse ntchito mbaula zamakono komanso kusintha zochitikachitika za makasitomala. Kubweretsa pamodzi kwa mbaula zamakono.

2.

Timagwiritsa ntchito njira zina zamakono mmalo mwa Makala ndi nkhuni zimene siziononga mitengo komanso sizipereka chiopsezo pa umoyo wathu. Zinthu zimene zikawolerana zimagwritsidwaso ntchito osati mitengo yamoyo yokha. Titha kuziotcha mmene zilili ngati njira yamakono mmalo mwa nkhuni kapena kuzisintha ku Makala, mabuliketi kapena mpweya.

Awa ndi maganizo ena:

Chifukwa chimene nsungwi zili zoyenerera kuthandizila zomera zina zomwe zimapereka mphamvu ndi choti zimatha kumeranso mwansanga malo amene zadulidwa.  Izi zikutanthauza kuti titha kukolola pafupipafupi tisanadule mtengo onse kusiyana ndi mitengo yomwe imatha kufa nthawi yomwe yadulidwa.

Kunena mwachindunji, nsungwi zimakula bwino kuno ku Malawi ndipo ziribe zovuta zambiri tikabwera ku mbali ya dothi ndi nyengo. Komabe mmene tingasamalilire mitengo yake zitha kuchititsa kuti mitengoyi ikule mwansanga ndi cholinga choti ikololedwe. Zaka zitatu kapena zisanu zimatha kukwana kuti zifike poyenera kukoloredwa ndi kuphukira mwansanga. Zidutswa zomwe timadula titha kuwumitsidwa kapena kuyatsidwa kuti zigwiritsidwe ntchito mmalo mwa nkhuni komanso Makala.

Mmalo mwa nkhuni titha kugwiritsanso ntchito zotsalira za zomera ndi chomera zina poziontcha mmene ziliri. Chitsanzo cha izi ndi mitengo ya Nandolo, thambi za mitengo komanso mapesi a chimanga. Mbaula zangati za chitetezo mbaula zimayaka bwino pogwiritsa ntchito tizidutswa tankhuni.

Ngati mlimi atha kudzala mahenji a nandolo mmbali mwa munda. Kupatula kupereka nkhuni pamakhala ubwino woonjezera ngati kuteteza kukokoloka kwa nthaka, kuteteza ku mphepo yoononga komanso imabweretsa zokudya zoyenerera mu nthaka ngati fetereza wachilengedwe.

Makala ndi oyipa pokhapokha ngati ataotchedwa kuchoka ku nkhuni zomwe sidadzalidwenso. Pali ndondomeko imodzi m’Malawi muno imene imapanga Makala okhazikika, izi zikutanthauza kuti mitengo imadzalidwa nthawi yomwe yadulidwa.

Mmene zalembedwera kale m’mwambamu titha kuotcha Makala kuchokera ku zomera zosiyanasiyana komanso nsungwi.

mabuliketsi ochokera ku zomera amapangidwa kugwiritsa ntchito zithulo zomwe zimasindikiza kwambiri zomerazi pozibweretsa pamodzi. Titha kugwiritsa ntchito zinthu zoonongeka zambiri monga matepala akutha, masamba a fodya, utuchi, ndowe za njovu, masamba a nthochi, makoko a mtedza, nyenyeswa za Makala ndi zotsalira za mbeu zina.  Titha kungotenga zinthu zimene ziri zopezekeratu mdera ndikuzisakaniza mwaluso. Ketengera ndi zinthu zomwe zagwiritsidwa ntchito, mmene zasindikizidwira komanso zinthu zina, ma buliketsi antha kukhala ndi mlingo osiyanasiyana oyatsila ndi nthawi yofanana komanso yabwinoko kusiyana ndi Makala. Zonsezi zimatha kuchitika posatulutsa utsi ofanana komanso posadula mitengo.

Uwu ndi mpweya omwe umapangidwa pamene zinyalala ndi zinthu zina zikuola pakugwiritsa ntchito bakiteriya amene amagwira ntchito malo amene okosijeni sapezeka. Zomera zomwe zimabweretsa mphamvu yophikira monga zotsalira zochokera mu ulimi ngati zotsalira mu mbewu, manyowa, mbeu zomwe zimapereka mphamvu komanso zidutswa za mbewu zakudimba, ndowe, zinyalala za m’mizinda komanso madzi owonongeka zimasiyidwa mu makontena amene salola mpweya kulowamo.  Tizilomboti sitifuna mpweya uliwose kuti tidye bwino zomerazi. Izi zikamachitika mpweya omwe umayaka kwambili otchedwa methane umapangidwa. Apatu titha kugwiritsa ntchito mpweyawu pophikira, kuunikira kapenanso kupangira magetsi. Ngati mpweyawu ukugwiritsidwira ntchito pophikira sumatulutsa utsi uliwonse ndipo nthawi zina umakhala ocheperako poyerekeza ndi mbaula zamakono. Njira yopanga mpweya umenewu imathandizaso mu ukhondo komanso kugwiritsa ntchito zinthu zonyansa. Mavuto amene akumapezeka pakugwiritsa ntchito njirayi popangira mpweya umenewu ndilakuti imafuna upangiri wapaderadera ndi ndalama yoyambira yochuluka.