Nthambo za magetsi zolumikizana mu ka dera kochepa ndi njira imene mphamvu ya magetsi imapangidwa pa mlingo ochepa (mlingo osafika ma mega watsi 10) ndipo nthambo zimenezi zimalumikizidwa ku ma dera amene sanalumikizidwe ku nthambo zopereka magetsi padziko (ESCOM) monga ku ma midzi. Njira imeneyi imagwira ntchito pa yokha posalumikizidwa ku nthambo zimene zimapereka magetsi pa dziko, choncho njirayi imatengedwa kukhala ya mtengo odalirika/otsikirako maka popereka magetsi ku ma dera a ku midzi omwe sanafikiridwe/sanalumikizidwe ndi nthambo zopereka magetsi pa dziko.

Malingana ndi bungwe lopanga mphamvu ya magetsi pa mlingo ochepa la Mulanje Electricity Generation Agency (MEGA), nthambo zolumikizidwa mu ka dera kochepa ndi zomwe zili zoyenera kwambiri ku madera omwe ali ndi chiwerengero cha anthu odutsa mazana awiri ndi makumi asanu (250) omwe akukhala mu dera la pafupifupi ma kilomita odutsa asanu kuchokera pa malo amene nthambo zopereka magetsi pa dziko zalumikizidwa. Potengera izi, ndizachidziwikire kuti nthambo zolumikizidwa zopereka magetsi mu ka dera kochepa ndi magetsi otsikirapo mtengo omwe ali oyenera kufikira chiwerengero cha a Malawi pafupifupi ma miliyoni okwanira 4.5, pamene pakadali pano ma peresenti okwanira 89 a Malawi m’dziko muno akukhala opanda magetsi. 

Ngakhale izi zili choncho, ma pulojekiti omwe akupanga mphamvu pa mlingo waung’ono m’dziko muno ndiochepa. Chitsanzo cha bwino ndi:

Nthambo zolumikizidwa zopereka magetsi mu ka dera kochepa pogwiritsa ntchito mphamvu ya madzi ku Mulanje:

Bungwe lopanga magetsi pa mlingo ochepa lotchedwa Mulanje Electricity Generation Agency (MEGA) linakhazikitsa chitukuko chopanga mphamvu kuchokera ku mphamvu ya madzi ndicholinga chofuna kupereka magetsi kapena mphamvu kwa anthu a ku midzi amene sadalumikizidwe ku nthambo zopereka magetsi pa dziko (ESCOM) pofuna kutula umoyo wa anthu ndi chuma.

M’mene chimakwana chaka cha 2018, makina opangira mphamvu yokwanira zikwi makumi asanu ndi limodzi (60kW) ndi omwe adakhazikitsidwa ndi nthambo zomwe zidalumikizidwa pa ma kilomita okwana makumi awiri (20km) anthu kapena ma kasitomala okwanira pafupifupi mazana atatu (300) adalumikizidwa ndi mphamvuyi. Ntchito imeneyi ikugwiridwa pakadali pano ikuonetsa kuonjezera kwa nyumba zina ziwiri zopangira mphamvu. Bungweli (MEGA) ndi limodzi mwa zitsanzo za bwino maka maka kumbali ya za malonda odalirika ndi okhazikika.

  • Kupanga Mphamvu: Magetsi atha kupangidwa kuchokera ku zinthu za chilengedwe zomwe ndi za m’bwezera kapena zomwe sizam’bwezere (zoziwikirapo ndi mphamvu ya: dzuwa, mphepo, madzi, zophikira zochokera ku zomera, mafuta ochokera ku zolengedwa zoola). Ntchito zachitukuko zimenezi zachepesa ndalama zomwe zimaonongeka ndikupereka mphamvu za unkhondo kwa anthu. Ntchito yopanga ndikugawa magetsi mukadera ka kang’ono imagwilitsa ntchito ngakhala kasakaniza wa mphamvu za m’bwezera.
  • Kusunga mphamvu: Malingana ndi kusintha-sintha kwa zinthu za chilengedwe za m’bwezera komaso kusintha-sintha kwa mlingo wa mphamvu yomwe ogula akonzeka kugula, ma batire ndiofunika kwambiri ndicholinga chofuna kusunga ndi kukhala ndi mphamvu yodalirika.
  • Kugawa: Magetsi opangidwa amatumizidwa kwa makasitomala ochepa kudzera m’mawaya omwe sadalumikizidwe ku nthambo zopereka magetsi pa dziko. Izi zikutanthauza nthambo kapena ma waya a moto wa magetsi ndi makina okuza ndi kuchepetsa mphamvu ya magetsi (tharanzifoma).
  • Nthambo zoyenelera zopereka magetsi mu ka dera kochepa: Titha kupititsa patsogolo njirayi poonjezera magawo amachitidwe osiyanasiyana monga kuika ayang’aniri oyenelera komaso kukhala osamalira.
  • Pofanizira ndi magetsi opangidwa pa mlingo ochuluka, magetsi olumikizidwa mu ka dera kakang’ono atha kukhala osavuta kulumikiza ndi kusamalira, amagwiritsidwa ntchito bwino komaso otsikirapo mtengo.
  • Nthambo zopereka magetsi mu ka dera kochepa zomwe zilibe vuto zimagwira ntchito bwino. Ndizodalirika, gwero lokhazikika la mphamvu, palibe kuzimazima kwa magetsi
  • Magetsi operekedwa mu ka dera kochepa opangidwa kuchokera ku mphamvu za m’bwezera ali ndi ubwino onse kumbali ya chilengedwe. Safuna dizilo popanga magetsi, amatulutsa mpweya oipa ochepa umene umafungatira mitambo.
  • Ubwino wake m’madera: Kupatula ubwino wa magetsi pa maphuznziro, chuma komanso pa za umoyo, magetsi operekedwa mu ka dera kochepa amapereka mwayi wa bwino kwa anthu potengapo mbali pa chitukuko cha m’madera.
  • Magetsi olumikizidwa mu ka dera kochepa ndi odalirika chifukwa ali ndi kuthekera kolumikizidwa ku nthambo zopereka magetsi pa dziko ndi cholinga choonjezera mphamvu imene ingagwiritsidwe ntchito mtsogolo.
  • Pali zinthu zoyenera kuunikiridwa m’ma dera ena maka pa nthambo zopereka magetsi mu ka dera kochepa zisanakhazikitsidwe monga, kutalika kwa ulendo kuchoka pa malo amene nthambo zopereka magetsi pa dziko zalumikizidwa, malo (okwera kapena otsika), kusankha gwero la mphamvu malingana ndi kusintha sintha kwa nyengo  
  • Kuti njirayi izigwira ntchito bwino, nthambo zopereka magetsi mu ka dera kochepa zikuyenera kukhazikitsidwa ndi ku samalidwa moyenelera. Izi zikutanthauza kuti pamafunika zipangizo zoyenera kumbali ya upangiri komanso chuma. Kusowekera kwa uyang’aniri wa bwino komaso kusasamalira kutha kudzetsa zotsatira zosakhala bwino.