Zipangizo zogwiritsa ntchito mphamvu yadzuwa zomwe zimayikidwa m’nyumba ndi njira yabwino yopangira magetsi posalumikizizana ndi nthambo zamagetsi za m’dziko. Mbale zokola mphamvu yadzuwa zimatha kugwiritsidwa ntchito pa chimbale chimodzi kapenanso zochulukirapo kuti zipange magetsi omwe atha kugwiritsidwa ntchito kuunikira ndi zinthu zina monga wailesi kapena kuonera kanema.

Zipangizo izi zimagwira ntchito pa mlingo wakatumizidwe kamoto wamagetsi okwanira mavoti khumi ndi mphambu ziwiri, motowu umakhala opita mbali imodzi pazipangizo zomwe zimagwiritsa ntchito moto ochepa kophatikizaponso chipangizo chomwe chimaongolera mlingo wa moto olowa mu batire ndinso pamakhala batire limodzi. Kutengera ndi mmene munthu akufunira pali zipangizo za mlingo ocheperako zimene zimakhala ngati poyambila kuchoka ku nyali za solar zatchedwa Pico kudzanso zazikulu zimene zimafunika akadaulo kuti zidzalidwe.

Wina mwa katundu amene amapezeka ku Malalwi wafotokozeredwa mmusimu:

Katundu wopezeka ku Malawi

Nyali za D20:

  • Mbale yokola mphamvu yadzuwa
  • Nyali ziwiri zokhala ndi suwitchi, nyale yonyamulika, mawaya okwanila ma mitala asanu ndi anayi ndi malo ulumikizira zinthu zina
  • Mpaka maola 15
  • Mtengo wake pafupifupi MK80,000

 

Chipangizo chamnyumba cha Jia H1:

  • Mbale yokola mphamvu yadzuwa yokwana ma wati asanu
  • Nyali ziwiri , batile yokhala ndi tochi , malo otchajira phone, wire onyamula moto wamagetsi okwana ma mita asanu
  • Walanti yokwana chaka

Makina otchedwa Sun King:

  • Mbale yokola mphamvu yadzuwa mpaka ma wati asanu ndi amodzi
  • Nyale zitatu zomwe zitha kupachikidwa komanso malo olumikizila mawaya otumizira uthenga
  • Kuwala kwa tsiku lonse ngati nyale yatchajidwa kwa tsiku lanthunthu
  • Malo osonyeza batile
  • Walanti yokwana zaka ziwiri
  • Mtengo pafupifupi MK63, 000

Makina a Connect 600:

  • Mbale za dzuwa zokola mphamvu zokwana ma wati asanu ndi chimodzi
  • Nyale zinayi, malo olumikizira zinthu, wailesi ndi fani
  • Dzaka dziwiri za walanti
  • Mtengo pafupifupi MK102, 000

Makina a ovSolar:

  • Mbale yopanga mphamvu yadzuwa zokwana ma wati asanu ndi atatu
  • Nyale zitatu zokhala ndi masuwitchi osiyana kuwala kwa maola asanu ndi mapoti okwana awiri.
  • Zaka ziwiri za chitsimikizo chogwiritsa ntchito asadaonongeke

Makina a Sundaya T-lite 2:

  • Mphamvu yadzuwa ya mmanyumba yomwe itha kuonjezeredwa
  • Mbale yokola mphamvu yadzuwa
  • Nyale zinayi zowala kwambiri ndi malo olumikiza malamya okwana anayi
  • Zimagulisilidwa mmalo ogulitsira mafuta a Total

Zuwa Kwacha 4:

  • Mbale zokola mphamvu yadzuwa yokwana ma wati khumi
  • Batile la mphamvu yokwana 3AH
  • Nyale zokwana zinayi, wailesi, tochi, mawaya komanso malo olumikiza zinthu zina
  • Yovomerezedwa ndi a Lighting Africa
  • Zaka ziwiri za chitsimikizo chogwiritsa ntchito mbale yadzuwa ndi zinthu zina zosungila moto
  • Mtego wokwana MK150,000
  • Kupereka mwapang’onopang’ono MK178,000, kuperekedwa pa miyezi khumi ndi mphambu zisanu ndi zitatu

Zuwa Kwacha 6:

  • Mbale zadzuwa zokola mphamvu yokwana ma wati khumi
  • Batile losunga moto okwana 3AH
  • Nyale zokwana zisanu ndi imodzi, wailesi, tochi, mawaya ndi thambo zosamutsira uthenga
  • Kuvomerezedwa ndi a Lightning Africa
  • Zaka ziwiri za walanti pa mbale yokola mphamvu ndi zina zosungira moto
  • Ndalama zogulira pafupifupi MK161,200
  • Kupereka mwa pang’onopang’ono ndi ndalama zokwana MK201,500 kwa miyezi khumi ndi mphambu zisanu ndi zitatu

Makina a Macheza:

  • Mbale zokola mphamvu yadzuwa yokwana ma wati makumi asanu ndi mphambu zisanu
  • Batire losunga moto okwana 12AH
  • Nyale zokwana zinayi, wayilesi ya kanema yamainchi khumi ndi mphamvu zisanu ndi zinayi yokhala ndi malo osamutsila zinthu, ma dekoda a Kiliye Kiliye, mawaya osamutsila moto, nthambo zosamutsila uthenga
  • Yovomerezeka ndi a Lightning Africa
  • Zaka ziwiri za walanti
  • Mtengo wa MK449 800
  • Kupereka pang’ono pang’ono ndi mtengo pafupifupi MK562200 kwa miyezi makumi awiri ndi mphambu ziwiri

Makina a Genus Solar Kit:

  • Mbale yokola mphamvu yadzuwa
  • Nyali ziwiri zokhala ndi suwitchi, nyale yonyamulika, mawaya okwanila ma mitala asanu ndi anayi ndi malo ulumikizira zinthu zina
  • Mpaka maola 15
  • Mtengo wake pafupifupi MK80,000