Nyumba yogulitsira magetsi ndi malo omwe magetsi amapangidwa ndicholinga chofuna kupereka njira zina zogwiritsa ntchito mphamvu monga kubwereketsa ma batire kapena nyali zogwiritsa ntchito mphamvu ya dzuwa, kutchaja ma foni ndi kuchita malonda ena monga malo ometera.

Kawiri kawiri nyumbayi imagwiritsa ntchito mbale zokoka mphamvu ya dzuwa, koma izi zitha kuthekaso pogwiritsa ntchito njira za mphamvu zina monga, mphamvu ya madzi kapena mphamvu ya mphepo. Mphamvuyi imasungidwa m’ma batire ndikugwiritsidwa ntchito moyenelera.

Ntchito zomwe zimapezeka pa nyumba yogulitsira magetsi ndi monga izi:

  • Malo otchajira: Anthu amatchajitsa zipangizo zawo zogwiritsa ntchito magetsi monga tochi, foni pa mtengo otsikirapo.
  • Kubwereketsa ma batire omwe atha kutchajidwaso pa nyumba ya magetsiyi ndi malo ogulitsira zipangizo za magetsi zodalirika monga ma tochi, ma babu a ma chubu kapena ma babu ogwiritsa ntchito mphamvu yochepa.
  • Kubwereketsa ndi kugulitsa ma babu ogwiritsa ntchito mphamvu ya dzuwa omwe ma kasitomala amatha kuloledwa kutenga pa ngongole ndikumabweza pang’onopang’ono
  • Ntchito zokhudza mphamvu: Malo ometera omwe amagwiritsa ntchito mphamvu ya dzuwa, makina owotchera chimanga cha mbuliuli (poposi), makina opangira chiponde ndi zina.
  • a nkumano, ochezera ndi kuthandizana maganizo a bwino opititsa chitukuko pa tsogolo

 

  • Nyumba zogulitsira magetsi zitha kukhala zokhazikika mu ntchito zake pogwilitsira ntchito ndalama zomwe akupeza polipira ogwira ntchito pa nyumbayi ndi ndalama zokonzetsera zipangizo zikaonongeka kudzera pobwereketsa ndi kugulitsa magetsi ndi zina. 
  • Imafuna ndalama yokhazikitsira yochepa kuchokera kwa makasitomala.  
  • Anthu a m’mudzi ndiwo amatengapo mbali. Zimayamba ndi anthu ogwira ntchito pa nyumbayi koma pamene ntchito ikupita patsogolo/ili nkati anthu atha kutengapo nawo mbali monga kupereka maganizo a kakhazikitsidwe ndi kakonzedwe ka makina ndi ukadaulo wa za malonda. Patha kukhala ubale wagwiro m’zipatala ndi m’ma sukulu ozungulira kapena malonda ang’onoang’ono okhazikika. Mwachisanzo, kulumikizana ndi omwe amapanga mbaula za makono, kupereka magetsi ku sukulu ndi m’zipatala. Mwayi ndi ochulukirachulukira ndipo pamene anthu adziwa ukadaulo pali kuthekera kwakulu/kochuluka kwa ntchito za chitukuko.
  • Pali njira zokhazikika pa mlingo wa ung’ono ngakhaleso pa mlingo wa ukulu.

Ndalama yokhazikitsira ndi yokonzera makina a m’nyumba yopanga magetsi ndiyokwera kwambiri maka kwa anthu okhala ku midzi. Kusintha kwa pulojekiti kuchoka m’manja mwa bungwe lothandiza ndikukhala chokhazikika ku anthu ndi vuto. Ntchito za chitukuko zambiri zimakhala zolephera kapena sizipita patsogolo pamene bungwe lothandiza lapereka ntchito ya chitukukoyi m’manja mwa anthu.